2 Natuma Eliyakimu woyang'anira nyumbayo, ndi Sebina mlembi, ndi akuru a ansembe opfundira ciguduli, kwa Yesaya mneneri mwana wa Amozi.
3 Nati kwa iye, Atero Hezekiya, Lero line ndilo tsiku la cisautso, ndi la kudzudzula, ndi la kunyoza; pakuti ana anafikira kubadwa, koma palibe mphamvu yakubala.
4 Kapena Yehova Mulungu wanu adzamva mau onse a kazembeyo, amene anamtuma mfumu ya Asuri mbuye wace, kuti atonze Mulungu wamoyo, nadzamlanga cifukwa ca mau adawamva Yehova Mulungu wanu; cifukwa cace uwakwezere otsalawo pemphero.
5 Ndipo anyamata a mfumu Hezekiya anafika kwa Yesaya.
6 Nanena nao Yesaya, Muzitero kwa mbuye wanu, Atero Yehova, Musamaopa mau mudawamva, amene anyamata a mfumu ya Asuri anandicitira nao mwano.
7 Taonani, ndidzalonga mwa iye mzimu wakuti adzamva mbiri, nadzabwerera kumka ku dziko lace, ndipo ndidzamgwetsa ndi lupanga m'dziko lace.
8 Nabwerera kazembeyo, napeza mfumu ya Asuri alikuthira nkhondo pa Libina, popeza anamva kuti adacoka ku Lakisi.