13 Ndipo Hezekiya anawamvera, nawaonetsa nyumba yonse ya cuma cace, siliva, ndi golidi, ndi zonunkhira, ndi mafuta okometsetsa, ndi nyumba ya zida zace, ndi zonse zopezeka pacuma pace; panalibe kanthu m'nyumba mwace, kapena m'ufumu wace wonse osawaonetsa Hezekiya.
14 Koma Yesaya mneneri anadza kwa mfumu Hezekiya, nati kwa iye, Anatani anthu awa? anadza kwa inu kufumira kuti? Nati Hezekiya, Afumira dziko la kutari ku Babulo.
15 Nati iye, Anaona ciani m'nyumba mwanu? Nati Hezekiya, Zonse za m'nyumba mwanga anaziona, palibe kanthu pacuma canga kosawaonetsa.
16 Ndipo Yesaya anati kwa Hezekiya, Tamverani mau a Yehova.
17 Taonani, akudza masiku kuti zonse za m'nyumba mwako, ndi zokundika makolo ako mpaka lero, zidzatengedwa kumka ku Babulo, kosasiyidwa kanthu konse, ati Yehova.
18 Nadzatenga ena a ana ako oturuka mwa iwe, amene udzawabala, nadzakhala iwo adindo m'cinyumba ca mfumu ya Babulo.
19 Pamenepo Hezekiya anati kwa Yesaya, Mau a Yehova udawanena ndi abwino. Natinso, Si momwemo nanga, mtendere ndi coonaeli zikakhala masiku anga?