16 Ndiponso Manase anakhetsa mwazi wambiri wosacimwa mpaka anadzaza m'Yerusalemu monsemo, osawerenga kulakwa kwace analakwitsa nako Yuda, ndi kucita coipa pamaso pa Yehova.
17 Macitidwe ena tsono a Manase, ndi zonse anazicita, sizilembedwa kodi m'buku la macitidwe a mafumu a Yuda?
18 Nagona Manase ndi makolo ace, naikidwa m'munda wa nyumba yace, m'munda wa Uza, nakhala mfumu m'malo mwace Amoni mwana wace.
19 Amoni anali wa zaka makumi awiri mphambu ziwiri polowa iye ufumu wace, nakhala mfumu zaka ziwiri m'Yerusalemu; ndi dzina la mace ndiye Mesulemeti mwana wa Haruzi wa ku Yotiba.
20 Nacita iye coipa pamaso pa Yehova, monga umo amacitira Manase atate wace.
21 Nayenda iye m'njira monse anayendamo atate wace, natumikira mafano anawatumikira atate wace, nawagwadira;
22 nasiya Yehova Mulungu wa makolo ace, sanayenda m'njira ya Yehova.