2 Nacita iye zoongoka pamaso pa Yehova, nayenda m'njira yonse ya Davide kholo lace, osapambukira ku dzanja lamanja kapena kulamanzere.
3 Ndipo kunali caka cakhumi mphambu zisanu ndi zitatu ca Yosiya, mfumuyi inatuma Safani mwana wa Azaliya mwana wa Mesulamu, mlembi, ku nyumba ya Yehova, ndi kuti,
4 Kwera kwa Hilikiya mkulu wa ansembe, awerenge ndalama zimene anthu anabwera nazo ku nyumba ya Yehova, ndizo zimene olindira pakhomo anasonkhetsa anthu; azipereke m'dzanja anchito akuyang'anira nyumba ya Yehova;
5 iwo azipereke kwa ogwira nchito ya m'nyumba ya Yehova, akonze mogamuka nyumbayi,
6 kwa amisiri a mitengo, ndi omanga nyumba, ndi omanga linga; ndi kuti agule mitengo ndi miyala yosema kukonza nazo nyumbayi.
7 Koma sanawawerengera ndalamazo zoperekedwa m'dzanja lao, pakuti anacita mokhulupirika.
8 Ndipo Hilikiya mkulu wa ansembe anati kwa Safani mlembi, Ndapeza buku la cilamulo m'nyumba ya Yehova. Napereka Hilikiya bukulo kwa Safani, iye naliwerenga.