17 Msinkhu wace wa nsanamira imodzi ndiwo mikono khumi mphambu isanu ndi itatu, ndi pamwamba pace mutu wamkuwa; ndi msinkhu wace wa mutuwo ndiwo mikono itatu, ndi ukonde, ndi makangaza pamutu pouzinga, zonse zamkuwa; ndi nsanamira inzace inali nazo zomwezo pamodzi ndi ukonde.
18 Ndipo mkuru wa olindirira anatenga Seraya wansembe wamkulu, ndi Zefaniya wansembe waciwiri, ndi olindira pakhomo atatu;
19 natenga m'mudzimo mdindo woikidwa woyang'anira ankhondo; ndi anthu asanu a iwo openya nkhope ya mfumu opezeka m'mudzimo; ndi mlembi, kazembe wa nkhondo wolembera anthu a m'dziko; ndi anthu a m'dziko makumi asanu ndi limodzi opezeka m'mudzimo.
20 Ndipo Nebuzaradani mkuru wa olindirira anawatenga, napita nao kwa mfumu ya Babulo ku Ribila.
21 Niwakantha mfumu ya Babulo, niwaphera ku Ribila m'dziko la Hamati. Motero anamuka nao Ayuda andende kuwacotsa m'dziko lao.
22 Koma kunena za anthu otsalira m'dziko la Yuda, amene adawasiya Nebukadinezara mfumu ya Babulo, iyeyu anamuika Gedaliya mwana wa Ahikamu mwana wa Safani akhale wowalamulira.
23 Ndipo pamene anamva akazembe onse a makamu, iwo ndi anthu ao, kuti mfumu ya Babulo adaika Gedaliya wowalamulira, anadza kwa Gedaliya ku Mizipa, ndiwo Ismayeli mwana wa Netaniya, ndi Yohanana mwana wa Kareya, ndi Seraya mwana wa Tanumeti wa ku Netofa, ndi Yazaniya mwana wa Mmakati, iwo ndi anthu ao omwe.