1 Ndipo Elisa ananena ndi mkazi uja adamuukitsira mwana wace, kuti, Nyamuka, numuke iwe ndi banja lako, nugonere komwe ukaone malo; pakuti Yehova waitana njala, nidzagwera dziko zaka zisanu ndi ziwiri.
2 Nanyamuka mkaziyo, nacita monga mwa mau a munthu wa Mulunguyo, namuka ndi banja lace, nagonera m'dziko la Afilisti zaka zisanu ndi ziwiri.
3 Ndipo pakutha pace pa zaka zisanu ndi ziwirizo, mkaziyo anabwera kucoka m'dziko la Afilisti, naturuka kukanena za nyumba yace ndi munda wace kwa mfumu.
4 Koma mfumu inalikulankhula ndi Gehazi mnyamata wa munthu wa Mulungu, ndi kuti, Ndifotokozere zazikuru zonse Elisa wazicita.