1 Ndipo Elisa ananena ndi mkazi uja adamuukitsira mwana wace, kuti, Nyamuka, numuke iwe ndi banja lako, nugonere komwe ukaone malo; pakuti Yehova waitana njala, nidzagwera dziko zaka zisanu ndi ziwiri.
2 Nanyamuka mkaziyo, nacita monga mwa mau a munthu wa Mulunguyo, namuka ndi banja lace, nagonera m'dziko la Afilisti zaka zisanu ndi ziwiri.
3 Ndipo pakutha pace pa zaka zisanu ndi ziwirizo, mkaziyo anabwera kucoka m'dziko la Afilisti, naturuka kukanena za nyumba yace ndi munda wace kwa mfumu.
4 Koma mfumu inalikulankhula ndi Gehazi mnyamata wa munthu wa Mulungu, ndi kuti, Ndifotokozere zazikuru zonse Elisa wazicita.
5 Ndipo kunali, alimkufotokozera mfumu m'mene adamuukitsira wakufayo, taonani, mkaziyo adamuukitisira mwana wace ananena za nyumba yace ndi munda wace kwa mfumu. Nati Gehazi, Mbuye wanga mfumu, suyu mkaziyo, suyu mwana wace Elisa anamuukitsayo?
6 Ndipo pofunsa mfumu, mkaziyo anaisimbira. Pamenepo mfumu anamuikira mdindo, ndi kuti, Bwezetsa zace zonse ndi zipatso zonse za m'munda, cicokere iye m'dziko mpaka lero lino.