8 Munthu amatamandidwa monga mwa nzeru yace;Koma wokhota mtima adzanyozedwa.
9 Wonyozedwa, amene ali ndi kapolo,Aposa wodzikuza, amene asowa zakudya.
10 Wolungama asamalira moyo wa coweta cace;Koma cifundo ca oipa ndi nkhanza.
11 Zakudyazikwanira wolima minda yace;Koma wotsata anthu opanda pace asowa nzeru.
12 Woipa akhumba cokodwa ndi amphulupulu;Koma muzu wa olungama umabala zipatso.
13 M'kulakwa kwa milomo muli msampha woipa;Koma wolungama amaturuka m'mabvuto.
14 Munthu amakhuta zabwino ndi zipatso za m'kamwa mwace;Zocita za manja ace zidzabwezedwa kwa iye.