8 Nsembe ya oipa inyansa Yehova;Koma pemphero la oongoka mtima limkondweretsa.
9 Njira ya oipa inyansa Yehova;Koma akonda wolondola cilungamo.
10 Wosiya njira adzalangidwa mowawa;Wakuda cidzudzulo adzafa.
11 Kumanda ndi kucionongeko kuli pamaso pa Yehova;Koposa kotani nanga mitima ya ana a anthu?
12 Wonyoza sakonda kudzudzulidwa,Samapita kwa anzeru.
13 Mtima wokondwa usekeretsa nkhope;Koma moyo umasweka ndi zowawa za m'mtima.
14 Mtima wa wozindikira ufunitsa kudziwa;Koma m'kamwa mwa opusa mudya utsiru.