1 POPEZA ambiri anayesa kulongosola nkhani ya zinthu zinacitika pakati pa ife,
2 monga anazipereka kwa ife iwo amene anakhala mboni ndi atumiki a mau,
3 kuyambira paciyambi, ndinayesa nkokoma inenso, amene ndinalondalonda mosamalitsa zinthu zonse kuyambira paciyambi, kulembera kwa iwe tsatane tsatane, Teofilo wabwinotu iwe;
4 kuti udziwitse zoona zace za mau amene unaphunzira.
5 Masiku a Herode, mfumu ya Yudeya, kunali munthu wansembe, dzina lace Zakariya, wa gulu la ansembe la Abiya; ndi mkazi wace wa ana akazi a pfuko la Aroni, dzina lace Elisabeti.
6 Ndipo onse awiri anali olungama mtima pamaso pa Mulungu, namayendabe m'malamulo onse ndi zoikika za Ambuye osacimwa.