13 Tsoka iwe, Korazini! tsoka iwe Betsaida! cifukwa kuti zikadacitika m'Turo ndi Sidoni zamphamvuzi zidacitika mwa inu, akadalapa kale lomwe ndi kukhala pansi obvala ciguduli ndi phulusa.
14 Koma ku Turo ndi Sidoni kudzapiririka m'ciweruziro, koposa inu.
15 Ndipo iwe, Kapernao, kodi udzakwezedwa kufikira Kumwamba? Udzatsitsidwa kufikira ku Hade,
16 iye wakumvera inu, andimvera Ine; ndipo iye wakukana inu, andikana Ine; ndipo iye wakukana Ine amkana iye amene anandituma Ine.
17 Ndipo makumi asanu ndi awiri aja anabwera mokondwera, nanena, Ambuye, zingakhale ziwanda zinatigonjera ife m'dzina lanu.
18 Ndipo anati kwa iwo, Ndinaona Satana alinkugwa ngati mphezi wocokera kumwamba.
19 Taonani, ndakupatsani ulamuliro wakuponda pa njoka ndi zinkhanira, ndi pa mphamvu iri yonse ya mdaniyo; ndipo kulibe kanthu kadzakuipsani konse.