17 Ndipo makumi asanu ndi awiri aja anabwera mokondwera, nanena, Ambuye, zingakhale ziwanda zinatigonjera ife m'dzina lanu.
18 Ndipo anati kwa iwo, Ndinaona Satana alinkugwa ngati mphezi wocokera kumwamba.
19 Taonani, ndakupatsani ulamuliro wakuponda pa njoka ndi zinkhanira, ndi pa mphamvu iri yonse ya mdaniyo; ndipo kulibe kanthu kadzakuipsani konse.
20 Koma musakondwera nako kuti mizimu idakugonjerani, koma kondwerani kuti maina anu alembedwa m'Mwamba.
21 Nthawi yomweyo iye anakondwera ndi Mzimu Wovera, nati, Ndikubvomerezani Inu, Atate, Ambuye wa kumwamba ndi wa dziko, kuti izi munazibisira anzeru ndi ozindikira, ndipo munaziululira ana amakanda; indedi, Atate, pakuti kotero kudakondweretsa pamaso panu.
22 Zonse zaperekedwa kwa Ine ndi Atate wanga; ndipo palibe munthu azindikira Mwana ali yani, koma Atate; ndipo Atate ali yani, koma Mwana, ndi iye amene Mwana afuna kumuululira iye.
23 Ndipo m'mene anapotolokera kwa ophunzira ace, ali pa okha, anati, Odala masowo akuona zimene muona.