1 Ndipo anakhalako nthawi yomweyo, anthu ena amene anamuuza iye za Agalileya, amene Pilato anasanganiza mwazi wao ndi nsembe zao.
2 Ndipo iye anayankha nati kwa iwo, Kodi muyesa kuti Agalileya aja anali anthu akucimwa koposa Agalileya onse, cifukwa anamva zowawa izi?
3 Ndinena kwa inu, iaitu; koma ngati inu simutembenuka mtima, mudzaonongeka nonse momwemo.
4 Kapena iwo aja khumi ndi asanu ndi atatu, amene nsanja yaitali ya m'Siloamu inawagwera, ndi kuwapha; kodi muyesa kuti iwo anali olakwa koposa anthu onse akukhala m'Yerusalemu?