1 Ndipo panali pamene iye analowa m'nyumba ya mmodzi wa akuru a Afarisi tsiku la Sabat a, kukadya, iwo analikumzonda iye.
2 Ndipo onani, panali pamaso pace munthu wambulu.
3 Ndipo Yesu anayankha nati kwa acilamulo ndi Afarisi, nanena, Kodi nkuloledwa tsiku la Sabata kuciritsa, kapena iai?
4 Koma iwo anakhala cete. Ndipo anamtenga namciritsa, namuuza apite.
5 Ndipo anati kwa iwo, Ndani wa inu buru wace kapena ng'ombe yace itagwa m'citsime, ndipo sadzaiturutsa pomwepo tsiku la Sabata kodi?
6 Ndipo iwo sanathe kumbwezera mau pa zinthu izi.
7 Ndipo iye ananena fanizo kwa oitanidwa, popenya kuti amadzisankhira mipando yaulemu, nanena kwa iwo,