3 Ndipo Yesu anayankha nati kwa acilamulo ndi Afarisi, nanena, Kodi nkuloledwa tsiku la Sabata kuciritsa, kapena iai?
4 Koma iwo anakhala cete. Ndipo anamtenga namciritsa, namuuza apite.
5 Ndipo anati kwa iwo, Ndani wa inu buru wace kapena ng'ombe yace itagwa m'citsime, ndipo sadzaiturutsa pomwepo tsiku la Sabata kodi?
6 Ndipo iwo sanathe kumbwezera mau pa zinthu izi.
7 Ndipo iye ananena fanizo kwa oitanidwa, popenya kuti amadzisankhira mipando yaulemu, nanena kwa iwo,
8 Pamene pali ponse waitanidwa iwe ndi munthu ku cakudya ca ukwati, usaseama pa mpando waulemu; kuti kapena wina waulemu wakuposa iwe akaitanidwe ndi iye,
9 ndipo pakufika iye amene adaitana iwe ndi uyu, adzati kwa iwe, Mpatse uyu malo; ndipo pomwepo udzayamba manyazi kukhala pa mpando wa kuthungo.