5 Ndipo anati kwa iwo, Ndani wa inu buru wace kapena ng'ombe yace itagwa m'citsime, ndipo sadzaiturutsa pomwepo tsiku la Sabata kodi?
6 Ndipo iwo sanathe kumbwezera mau pa zinthu izi.
7 Ndipo iye ananena fanizo kwa oitanidwa, popenya kuti amadzisankhira mipando yaulemu, nanena kwa iwo,
8 Pamene pali ponse waitanidwa iwe ndi munthu ku cakudya ca ukwati, usaseama pa mpando waulemu; kuti kapena wina waulemu wakuposa iwe akaitanidwe ndi iye,
9 ndipo pakufika iye amene adaitana iwe ndi uyu, adzati kwa iwe, Mpatse uyu malo; ndipo pomwepo udzayamba manyazi kukhala pa mpando wa kuthungo.
10 Koma pamene pali ponse waitanidwa iwe, pita nukhale pansi pa malo a kuthungo; kotero kuti pamene akadza iye anakuitana iwe, akanena ndi iwe, Bwenzi langa, sendera, kwera kuno; pomwepo udzakhala ndi ulemerero pamaso pa onse akuseama pacakudya pamodzi ndi iwe.
11 Cifukwa munthu ali yense wakudzikuza adzacepetsedwa; ndipo wakudzicepetsa adzakulitsidwa.