1 Koma amisonkho onse ndi anthu ocimwa analikumyandikira kudzamva iye.
2 Ndipo Afarisi ndi alembi anadandaula nati, Uyu alandira anthu ocimwa, nadya nao.
3 Koma anati kwa iwo fanizo ili, nanena,
4 Munthu ndani wa inu ali nazo nkhosa makumikhumi, ndipo pakutayika imodzi ya izo, sasiya nanga m'cipululu zinazo makumi asanu ndi anai mphambu zisanu ndi zinai, nalondola yotayikayo kufikira aipeza?
5 Ndipo pamene adaipeza, aisenza pa mapewa ace wokondwera.
6 Ndipo pakufika kunyumba kwace amema abwenzi ace ndi anansi ace, nanena nao, Kondwerani ndi ine, cifukwa ndinapeza nkhosa yanga yotayikayo.
7 Ndinena kwa inu, kotero kudzakhala cimwemwe Kumwamba cifukwa ca wocimwa mmodzi wotembenuka mtima, koposa anthu olungama makumi asanu ndi anai mphambu asanu ndi anai, amene alibe kusowa kutembenuka mtima.