21 ndipo anafuna kukhuta ndi zakugwa pa gome la mwini cumayo; komatu agarunso anadza nanyambita zirondazace.
22 Ndipo kunali kuti wopemphayo adafa, ndi kuti anatengedwa iye ndi angelo kunka ku cifuwa ca Abrahamu; ndipo mwini cumayo adafanso, naikidwa m'manda.
23 Ndipo m'Hade anakweza maso ace, pokhala nao mazunzo, naona Abrahamu patali, ndi Lazaro m'cifuwa mwace.
24 Ndipo anakweza mau nati, Atate Abrahamu, mundicitire cifundo, mutome Lazaro, kuti abviike nsonga ya cala cace m'madzi, naziziritse lilime langa; pakuti ndizunzidwadi m'lawi ili la moto.
25 Koma Abrahamu anati, Mwana, kumbukila kuti unalandira zokoma zako pakukhala m'moyo iwe, momwemonso Lazaro zoipa; ndipo tsopano iye asangalatsidwa pano, koma iwe uzunzidwadi.
26 Ndipo pamwamba pa izi, pakati pa ife ndi inu pakhazikika phompho lalikuru, kotero kuti iwo akufuna kuoloka kucokera kuno kunka kwa inu sangathe, kapena kucokera kwanuko kuyambuka kudza kwa ife, sangathenso.
27 Koma anati, Pamenepo ndikupemphani, Atate, kuti mumtume ku nyumba ya atate wanga;