25 Ndipo onani, m'Yerusalemu munali munthu, dzina lace Simeoni; ndipo munthu uyu, wolungama mtima ndi wopemphera, analikulindira matonthozedwe a Israyeli; ndipo Mzimu Woyera anali pa iye.
26 Ndipo anamuululira Mzimu Woyera kuti sadzaona imfa, kufikira adzaona Kristu wace wa Ambuye.
27 Ndipo iye analowa kuKacisi ndi Mzimu: ndipo pamene atate ndi amace analowa ndi kamwanako Yesu, kudzamcitira iye mwambo wa cilamulo,
28 pomwepo iye anamlandira iye m'manja mwace, nalemekeza Mulungu, nati,
29 Tsopano, Ambuye, monga mwa mau anu aja,Lolani ine, kapolo wanu, ndicoke mumtendere;
30 Cifukwa maso anga adaona cipulumutso canu,
31 Cimene munakonza pamaso pa anthu onse,