38 Ndipo iye anafikako pa nthawi yomweyo, nabvomerezanso kutama Mulungu, nalankhula za iye kwa anthu onse 1 akuyembekeza ciombolo ca Yerusalemu.
39 Ndipo pamene iwo anatha zonse monga mwa cilamulo ca Ambuye, anabwera ku Galileya, ku mudzi kwao, ku Nazarete.
40 Ndipo 2 mwanayo anakula nalimbika, nalikudzala ndi nzeru; ndi cisomo ca Mulungu cinali pa iye.
41 Ndipo atate wace ndi amace 3 akamuka caka ndi caka ku Yerusalemu ku Paskha.
42 Ndipo pamene iye anakhala ndi zaka zace khumi ndi ziwiri, anakwera iwo monga macitidwe a phwando;
43 ndipo pakumariza masiku ace, pakubwera iw, mnyamatayo Yesu anatsala m'mbuyo ku Yerusalemu. Ndipo atate ndi amace sanadziwa;
44 koma iwo anayesa kuti iye ali m'cipiringu ca ulendo, nayenda ulendo wa tsiku limodzi; ndipo anayamba kumfunafuna iye mwa abale ao ndi mwa anansi ao;