29 Tsono panali abale asanu ndi awiri; ndipo woyamba anakwatira mkazi, nafa wopanda mwana;
30 ndipo waciwiri,
31 ndi wacitatu anamtenga mkaziyo; ndipo coteronso asanu ndi awiri onse, sanasiya mwana, namwalira.
32 Pomarizira anamwaliranso mkaziyo.
33 Potero m'kuuka iye adzakhala mkazi wa yani wa iwo? pakuti asanu ndi awiriwo adamkwatira iye.
34 Ndipo Yesu anati kwa iwo, Ana a dziko lapansi akwatira nakwatiwa:
35 koma iwo akuyesedwa oyenera kufikira dzikolijalo, ndi kuuka kwa akufa, sakwatira kapena kukwatiwa.