25 Ndipo kudzakhala zizindikilo pa dzuwa ndi mwezi ndi nyenyezi; ndi pa dziko lapansi cisauko ca mitundu ya anthu, alikuthedwa nzeru pa mkukumo wace wa nyanja ndi mafunde ace;
26 anthu akukomoka ndi mantha, ndi kuyembekeeera zinthu zirinkudza ku dziko lapansi;
27 pakuti mphamvu zakumwamba zidzagwedezeka. Ndipo pamenepo adzaona Mwana wa munthu alinkudza mu mtambo ndi mphamvu ndi ulemerero waukuru.
28 Komapoyamba kucitika izi weramukani, tukulani mitu yanu; cifukwa ciomboledwe canu cayandikira.
29 Ndipo ananena nao fanizo; Onani mkuyu, ndi mitengo yonse:
30 pamene iphukira, muipenya nimuzindikira pa nokha kuti dzinja liri pafupi pomwepo.
31 Inde cotero inunso, pakuona zinthu izi zirikucitika, zindikirani kuti Ufumu wa Mulungu uli pafupi.