12 Ndipo iyeyo adzakuonetsani cipinda cacikuru capamwamba, cokonzeka; mukakonzere kumeneko.
13 Ndipo anapita iwo, napeza monga adatero nao; ndipo anakonza Paskha.
14 Ndipo itadza nthawi yace, iye anakhala pacakudya, ndi ophunzira pamodzi ndi iye.
15 Ndipo anati kwa iwo, Ndinalakalaka ndithu kudya Paskha uwu pamodzi ndinu, ndisanayambe kusautsidwa;
16 pakuti ndinena ndi inu, sindidzadya kufikira udzakwaniridwa mu Ufumu wa Mulungu.
17 Ndipo analandira cikho, ndipo pamene adayamika, anati, Landirani ici, mucigawane mwa inu nokha;
18 pakuti ndinena kwa inu, kuyambira tsopano Ine sindidzamwako cipatso ca mpesa, kufikira Ufumu wa Mulungu udzafika.