21 Koma onani, dzanja lace la iye amene adzandipereka ali pagome pano pamodzi ndi Ine.
22 Pakuti Mwana wa munthu amukatu, monga kunaikidwiratu; koma tsoka munthuyo amene ampereka!
23 Ndipo anayamba kufunsana mwa iwo okha, ndiye yani mwa iwo amene adzacita ici.
24 Ndipo kunakhala kutsutsana mwa iwo, ndani wa iwo ayesedwe wamkuru.
25 Ndipo anati kwa iwo, Mafumu a anthu a mitundu awacitira ufumu; ndipo iwo amene awacitira ulamuliro anenedwa, Ocitira zabwino.
26 Koma sipadzatero ndi inu; komatu iye ali wamkuru mwa inu, akhale ngati wamng'ono; ndi iye ali woyamba, akhale ngati wotumikira.
27 Pakuti wamkuru ndani, iye wakuseama pacakudya kapena wakutumikirapo? si ndiye wakuseama pacakudya kodi? koma Ine ndiri pakati pa inu monga ngati wotumikira.