3 Ndipo Satana analowa m'Yudase wonenedwa Isikariote, amene anawerengedwa mmodzi wa khumi ndi awiriwo,
4 Ndipo iye anacoka, nalankhulana ndi ansembe akulu ndi akazembe mompereka iye kwa iwo.
5 Ndipo anakondwera, napangana naye kumpatsa ndalama.
6 Ndipo iye anabvomera, nafunafuna nthawi yabwino yakumpereka iye kwa iwo, pakalibe khamu la anthu.
7 Ndipo tsiku la mikate yopanda cotupitsa linafika, limene inayenera kuphedwa nsembe ya Paskha.
8 Ndipo iye anatumiza Petro ndi Yohane, nati, Pitanimutikonzere ife Paskha, kuti tidye.
9 Ndipo iwo ananena naye, Mufuna tikakonzere kuti?