1 Ndipo kunali tsiku la Sabata, iye analinkupita pakati pa minda ya tirigu; ndipo ophunzira ace analinkubudula ngala za tirigu, nazifikisa m'manja mwao, nadya.
2 Koma Afarisi ena anati, Mucitiranji cosaloledwa kucitika tsiku la Sabata?
3 Ndipo Yesu anayankha nati kwa iwo, Kodi simunawerenganso ngakhale cimene anacita Davine, pamene paja anamva Njala, iye ndi iwo anali naye pamodzi,
4 kuti analowa m'nyumba ya Mulungu, natenga mikate yoonetsera, nadya, napatsanso iwo anali naye pamodzi; imeneyi yosaloledwa kudya ena koma ansembe okha?