16 ndi Yuda mwana wa Yakobo, ndi Yudase Isikariote, amene anali wompereka iye.
17 Ndipo iye anatsika nao, naima pacidikha, ndi khamu lalikuru la ophunzira ace, nw unyinji waukuru wa anthu a ku Yudeya lonse ndi Yerusalemu, ndi a ku mbali ya nyanja ya ku Turo ndi Sidoni, amene anadza kudzamva iye ndi kudzaciritsidwa nthenda zao;
18 ndipo obvutidwa ndi mizimu yonyansa anaciritsidwa,
19 ndi khamu lonse lija linafuna kumkhudza iye; cifukwa munaturuka mphamvu mwa iye, niciritsa onsewa.
20 Ndipo iye anakweza maso ace kwa ophunzira ace, nanena, Odala osauka inu; cifukwa uli wanu ufumu wa Mulungu.
21 Odala inu akumva njala tsopano; cifukwa mudzakhuta. Odala inu akulira tsopano; cifukwa mudzaseka.
22 Odala inu, pamene anthu adzada inu, nadzapatula inu, nadzatonza inu, nadzalitaya dzina lanu monga loipa, cifukwa ca Mwana wa munthu.