18 ndipo obvutidwa ndi mizimu yonyansa anaciritsidwa,
19 ndi khamu lonse lija linafuna kumkhudza iye; cifukwa munaturuka mphamvu mwa iye, niciritsa onsewa.
20 Ndipo iye anakweza maso ace kwa ophunzira ace, nanena, Odala osauka inu; cifukwa uli wanu ufumu wa Mulungu.
21 Odala inu akumva njala tsopano; cifukwa mudzakhuta. Odala inu akulira tsopano; cifukwa mudzaseka.
22 Odala inu, pamene anthu adzada inu, nadzapatula inu, nadzatonza inu, nadzalitaya dzina lanu monga loipa, cifukwa ca Mwana wa munthu.
23 Kondwerani tsiku lomweli, tumphani ndi cimwemwe; pakuti onani, mphotho zanu nzazikuru Kumwamba; pakuti makolo ao anawacitira aneneri zonga zomwezo.
24 Koma tsoka inu eni cuma! cifukwa mwalandira cisangalatso canu.