2 Koma Afarisi ena anati, Mucitiranji cosaloledwa kucitika tsiku la Sabata?
3 Ndipo Yesu anayankha nati kwa iwo, Kodi simunawerenganso ngakhale cimene anacita Davine, pamene paja anamva Njala, iye ndi iwo anali naye pamodzi,
4 kuti analowa m'nyumba ya Mulungu, natenga mikate yoonetsera, nadya, napatsanso iwo anali naye pamodzi; imeneyi yosaloledwa kudya ena koma ansembe okha?
5 Ndipo iye ananena kwa iwo, kuti, Mwana wa munthu ali Mbuye wa tsiku la Sabata.
6 Ndipo kunali tsiku lina la Sabata, iye analowa m'sunagoge naphunzitsa. Ndipo munali munthu momwemo, ndipo dzanja lace lamanja linali lopuwala.
7 Ndipo alembi ndi Afarisi analikumzonda iye, ngati adzaciritsa tsiku la Sabata; kuti akapeze comneneza iye.
8 Koma iye anadziwa maganizo ao; nati kwa munthuyo wa dzanja lace lopuwala, Nyamuka, nuimirire pakatipo.