35 Koma 3 takondanani nao adani anu, ndi kuwacitira zabwino, ndipo kongoletsani osayembekeza kanthu konse, ndipo mphotho yanu idzakhala yaikuru, ndipo 4 inu mudzakhala ana a Wamkurukuruyo; cifukwa iye acitira zokoma anthu osayamika ndi oipa.
36 Khalani inu acifundo monga Atate wanu ali wacifundo. Ndipo musamaweruza, ndipo simudzaweruzidwa.
37 Ndipo 5 musawatsutsa, ndipo simudzatsutsidwa. Masulani, ndipo mudzamasulidwa.
38 6 Patsani, ndipo kudzapatsidwa kwa inu; muyeso wabwino, wotsendereka, wokucumuka, wosefukira, anthu adzakupatsani m'manja mwanu. Pakuti 7 kudzayesedwa kwa inu ndi muyeso womwewo muyesa nao inu.
39 Ndipo iye ananenanso nao fanizo, 8 Kodi munthu wakhungu angathe kutsogolera mnzace wakhungu? kodi sadzagwa onse awiri m'mbuna?
40 9 Wophunzira saposa mphunzitsi wace; koma yense, m'mene atakonzedwa mtima, adzafanana ndi mphunzitsi wace.
41 Ndipo uyang'aniranji kacitsotso kali m'diso la mbale wako, koma mtanda wa m'diso la iwe mwini suuzindikira?