14 Ndipo yemwe sadzakulandirani inu, kapena kusamva mau anu, pamene mulikuturuka m'nyumbayo, kapena m'mudzimo, sansani pfumbi m'mapazi anu.
15 Indetu ndinena kwa inu, kuti, tsiku la kuweruza, mlandu wao wa Sodomu ndi Gomora udzacepa ndi wace wa mudzi umenewo.
16 Taonani, Ine ndikutumizani inu monga nkhosa pakati pa afisi; cifukwa cace khalani ocenjera monga njoka, ndi oona mtima monga nkhunda.
17 Koma cenjerani ndi anthu; pakuti adzakuperekani inu kwa akuru a mlandu, nadzakukwapulani inu m'masunagoge mwao;
18 Ndiponso adzamuka nanu kwa akazembe ndi mafumu cifukwa ca Ine, kukhala mboni ya kwa iwo, ndi kwa anthu akunja.
19 Koma pamene pali ponse angakuperekeni inu, musamadera nkhawa mudzalankhule bwanji kapena mudzanene ciani; pakuti cimene mudzacilankhula, cidzapatsidwa kwa inu nthawi yomweyo;
20 pakuti wolankhula si ndinu, koma Mzimu wa Atate wanu akulankhula mwa inu.