17 Koma cenjerani ndi anthu; pakuti adzakuperekani inu kwa akuru a mlandu, nadzakukwapulani inu m'masunagoge mwao;
18 Ndiponso adzamuka nanu kwa akazembe ndi mafumu cifukwa ca Ine, kukhala mboni ya kwa iwo, ndi kwa anthu akunja.
19 Koma pamene pali ponse angakuperekeni inu, musamadera nkhawa mudzalankhule bwanji kapena mudzanene ciani; pakuti cimene mudzacilankhula, cidzapatsidwa kwa inu nthawi yomweyo;
20 pakuti wolankhula si ndinu, koma Mzimu wa Atate wanu akulankhula mwa inu.
21 Ndipo mbale adzapereka mbale wace kuimfa, ndi atate mwana wace: ndipo ana adzatsutsa akuwabala, nadzawafetsa iwo.
22 Ndipo adzada inu anthu onse cifukwa ca dzina langa; koma iye wakupirira kufikira cimariziro, iyeyu adzapulumutsidwa.
23 Koma pamene angakuzunzeni inu m'mudzi uwu, thawirani mwina: indetu ndinena kwa inu, Simudzaitha mizinda ya Israyeli, kufikira Mwana wa munthu atadza.