20 pakuti wolankhula si ndinu, koma Mzimu wa Atate wanu akulankhula mwa inu.
21 Ndipo mbale adzapereka mbale wace kuimfa, ndi atate mwana wace: ndipo ana adzatsutsa akuwabala, nadzawafetsa iwo.
22 Ndipo adzada inu anthu onse cifukwa ca dzina langa; koma iye wakupirira kufikira cimariziro, iyeyu adzapulumutsidwa.
23 Koma pamene angakuzunzeni inu m'mudzi uwu, thawirani mwina: indetu ndinena kwa inu, Simudzaitha mizinda ya Israyeli, kufikira Mwana wa munthu atadza.
24 Wophunzira saposa mphunzitsi wace, kapena kapolo saposa mbuye wace.
25 Kumkwanira wophunzira kuti akhale monga mphunzitsi wace, ndi kapolo monga mbuye. Ngati anamucha mwini banja Beelzebule, sadzaposa kodi kuwatero apabanja ace?
26 Cifukwa cace musaopa iwo; pakuti palibe kanthu kanabvundikiridwa, kamene sikadzaululidwa; kapena kanthu kobisika, kamene sikadzadziwika.