1 Ndipo panali, pamene Yesu anatha kuwafotokozera ophunzira ace khumi Ndi awiri, Iye anacokera kumeneko kukaphunzitsa Ndi kulalikira m'midzi mwao.
2 Koma Yohane, pakumva m'nyumba yandende nchito za Kristu, anatumiza ophunzira ace mau,
3 nati kwa Iye, Inu ndinu wakudza kodi, kapena tiyembekezere wina?
4 Ndipo Yesu anayankha, nanena nao, Mukani mubwezere mau kwa Yohane zimene muzimva ndi kuziona:
5 akhungu alandira kuona kwao, Ndi opunduka miyendo ayenda, akhate akonzedwa, indi ogontha akumva, ndi akufa aukitsidwa, ndi kwa aumphawi ulalikidwa uthenga wabwino.