11 Indetu ndinena kwa inu, Sanauke wakubadwa mwa akazi munthu wamkuru woposa Yohane Mbatizi; koma iye amene ali wocepa mu Ufumu wa Kumwamba amkulira iye.
12 Ndipo kuyambira masiku a Yohane Mbatizi, kufikira tsopano lino, Ufumu wa Kumwamba uli wokangamizidwa, ndipo okangamirawo aukwatula ndi mphamvu.
13 Pakuti aneneri onse ndi cilamulo cinanenera kufikira pa Yohane.
14 Ndipo ngati mufuna kulandira, uyu ndiye Eliya amene amati akudza.
15 Amene ali ndi makutu akumva, amve.
16 Koma ndidzafanizira ndi ciani obadwa awa a makono? Ali ofanana ndi ana akukhala m'mabwalo a malonda, amene alikuitana anzao,
17 ndi kuti, Tinakulizirani inu zitoliro, ndipo inu simunabvina; tinabuma maliro, ndipo inu simunalira.