14 Ndipo ngati mufuna kulandira, uyu ndiye Eliya amene amati akudza.
15 Amene ali ndi makutu akumva, amve.
16 Koma ndidzafanizira ndi ciani obadwa awa a makono? Ali ofanana ndi ana akukhala m'mabwalo a malonda, amene alikuitana anzao,
17 ndi kuti, Tinakulizirani inu zitoliro, ndipo inu simunabvina; tinabuma maliro, ndipo inu simunalira.
18 Pakuti Yohane anadza wosadya, wosamwa, ndipo iwo amati, Ali ndi ciwanda.
19 Mwana wa munthu anadza wakudya, ndi wakumwa, ndipo iwo amati, Onani munthu wakudyaidya ndi wakumwaimwa vinyo, bwenzi la amisonkho ndi ocimwa! Ndipo nzeru iyesedwa yolungama ndi nchito zace.
20 Pomwepo Iye anayamba kutonza midziyo, m'mene zinacitidwa zambiri za nchito zamphamvu zace, cifukwa kuti siinatembenuke.