4 Ndipo Yesu anayankha, nanena nao, Mukani mubwezere mau kwa Yohane zimene muzimva ndi kuziona:
5 akhungu alandira kuona kwao, Ndi opunduka miyendo ayenda, akhate akonzedwa, indi ogontha akumva, ndi akufa aukitsidwa, ndi kwa aumphawi ulalikidwa uthenga wabwino.
6 Ndipo wodala iye amene sakhumudwa cifukwa ca Ine.
7 Ndipo m'mene iwo analikumuka, Yesu anayambonena Ndi makamu a anthu za kwa Yohane, Munaturuka kunka kucipululu kukapenyanji? Bango logwedezeka nd: mphepo kodi?
8 Koma munaturuka kukaona ciani? Munthu wobvala zofewa kodi? Onani, akubvala zofewa alim'nyumba zamafumu.
9 Koma munaturukiranji? Kukaona mneneri kodi? Indetu, ndinena kwa inu, wakuposa mneneri.
10 Uyu ndiye amene kunalembedwa za iye, kuti,Onani Ine nditumiza mthenga wanga pa nkhope yanu,Amene adzakonza njira yanu m'tsogolo mwanu.