26 Koma pamene mmera unakula, nubala cipatso, pomwepo anaonekeranso namsongole.
27 Ndipo anyamata ace a mwini nyumbayo anadza, nati kwa iye, Mbuye, kodi simunafesa mbeu zabwino m'munda mwanu? nanga wacokera kuti namsongoleyo?
28 Ndipo iye ananena kwa iwo, Munthu mdani wanga wacicita ici. Ndipo anyamata anati kwa iye, Kodi mufuna tsopano kuti timuke, tikamsonkhanitse uyo pamodzi?
29 Koma iye anati, lai, kuti kapena m'mene mukasonkhanitsa namsongoleyo, mungazulenso tirigu pamodzi naye.
30 Kazilekeni zonse ziwiri, zikulire pamodzi kufikira pakututa; ndimo m'nyengo yakututa ndidzauza akututawo, Muyambe kusonkhanitsa namsongole, mummange uyu mitolo kukamtentha, koma musonkhanitse tirigu m'nkhokwe yanga.
31 Fanizo lina Iye anawafotokozera iwo, nanena, Ufumu wa Kumwamba uli wofanafana ndi kambeu kampiru, kamene anakatenga munthu, nakafesa pamunda pace;
32 kamene kakhaladi kakang'ono koposa mbeu zonse, koma katakula, kali kakakuru kuposa zitsambazonse, nukhala mtengo, kotero kuti mbalame za mlengalenga zimadza, nizibindikira mu nthambi zace.