13 Ndipo Yesu pakumva, anacokera kumeneko m'ngalawa, kunka ku malo acipululu pa yekha; ndipo makamu, pamene anamva, anamtsata Iye mumtunda kucokera m'midzi.
14 Ndipo Iye anaturuka, naona khamu lalikuru la anthu, nacitira iwo cifundo, naciritsa akudwala ao.
15 Ndipo pamene panali madzulo, ophunzira ace anafika kwa Iye, nanena, Malo ano nga cipululu, ndipo nthawi yapita tsopano; kauzeni makamuwo amuke, apite ku midzi kukadzigulira okha kamba.
16 Koma Yesu anati kwa iwo, Iwo alibe cifukwa ca kumukira, apatseni ndinu adye.
17 Koma iwo ananena kwa Iye, Ife tiribe kanthu pano koma mikate isanu, ndi nsomba ziwiri.
18 Ndipo Iye anati, Mudze nazo kuno kwa Ine.
19 Ndipo Iye analamulira makamu a anthu akhale pansi pamaudzu; ndipo Iye anatenga mikate isanuyo ndi nsomba ziwirizo, ndipo m'mene anayang'ana kumwamba, anadalitsa, nanyema, napatsa mikateyo kwa ophunzira, ndi ophunzira kwa makamuwo.