27 Ndipo mbuye wa kapoloyo anagwidwa ndi cisoni mumtima, nammasula iye, namkhululukira ngongole.
28 Koma kapolo uyu, poturuka anapeza wina wa akapolo anzace yemwe anamkongola iye marupiya atheka makumi khumi, namgwira, namkanyanga pakhosi, nati, Bwezera cija unacikongola.
29 Pamenepo kapolo mnzaceyu anagwada pansi, nampempha iye, nati, Bakandiyembekeza ine, ndipo ndidzakubwezera.
30 Ndipo iye sanafuna; koma anamuka, namponya iye m'nyumba yandende, kufikira abwezere ngongole.
31 Cifukwa cace m'mene akapolo anzace anaona zocitidwazo, anagwidwa cisoni cacikuru, nadza, nalongosolera mbuye wao zonse zimene zinacitidwa.
32 Pomwepo mbuye wace anamuitana iye, nanena naye, Kapolo iwe weipa, ndinakukhululukira iwe mangawa onse aja momwe muja unandipempha ine;
33 kodi iwenso sukadamcitira kapolo mnzako cisoni, monga inenso ndinakucitira iwe cisoni?