23 Ndipo Yesu anati kwa ophunzira ace, Indetu ndinena kwa inu, kuti munthu mwini cuma adzalowa mobvutika mu Ufumu wa Kumwamba.
24 Ndiponso ndinena kwa inu, Nkwapafupi kuti ngamila ipyole diso la singano, koposa mwini cuma kulowa Ufumu wa Kumwamba.
25 Ndipo ophunzira, pamene anamva, anazizwa kwambiri, nanena, Ngati nkutero angapulumuke ndani?
26 Ndipo Yesu anawayang'ana, nati kwa iwo, ici sicitheka ndi anthu, koma zinthu zonse zitheka ndi Mulungu.
27 Pomwepo Petro anayankha, nati kwa Iye, Onani, ife tinasiya zonse ndi kutsata Inu; nanga tsono tidzakhala ndi ciani?
28 Ndipo Yesu anati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, kuti inu amene munanditsata Ine, m'kubadwanso, pamene Mwana wa munthu adzakhala pa cimpando ca ulemerero wace, inunso, mudzakhala pa mipando khumi ndi iwiri, kuweruza mafuko khumi ndi awiri a Israyeli.
29 Ndipo onse amene adasiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena atate, kapena amai, kapena ana, kapena minda, cifukwa ca dzina langa, adzalandira zobwezeredwa zambirimbiri, nadzalowa moyo wosatha.