3 Ndipo Afarisi anadza kwa Iye, namuyesa, nanena, Kodi nkuloledwa kuti munthu acotse mkazi wace pa cifukwa ciri conse?
4 Ndipo Iye anayankha, nati, Kodi simunawerenga kuti Iye amene adalenga anthu paciyambi, anawalenga iwo mwamuna ndi mkazi,
5 nati, Cifukwa ca ici mwamuna adzasiya atate wace ndi amace, nadzaphatikizana ndi mkazi wace, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi?
6 cotero kuti salinso awiri koma thupi limodzi. Cifukwa cace ici cimene Mulungu anacimanga pamodzi, munthu asacilekanitse.
7 Iwo ananena kwa Iye, Nanga cifukwa ninji Mose analamulira kupatsa kalata wa cilekaniro, ndi kumcotsa?
8 Iye ananena kwa iwo, Cifukwa ca kuuma mtima kwanu, Mose anakulolezani kucotsa akazi anu; koma paciyambi sikunakhala comweco.
9 Ndipo Ine ndinena kwa inu, Amene ali yense akacotsa mkazi wace, kosakhala cifukwa ca cigololo, nadzakwatira wina, acita cigololo: ndipo iye amene akwatira wocotsedwayo, acita cigololo.