10 Ndipo m'mene adalowa m'Yerusalemu mudzi wonse unasokonezeka, nanena, ndani uyu?
11 Ndipo makamu a anthu anati, Uyu ndi mneneri Yesu wa ku Nazarete wa ku Galileya.
12 Ndipo Yesu analowa ku Kacisi wa Mulungu naturutsira kunja onse akugulitsa ndi kugula malonda, nagubuduza magome a osintha ndalama, ndi mipando ya ogulitsa nkhunda;
13 nanena kwa iwo, Calembedwa, Nyumba yanga idzanenedwa nyumba yakupemphera; koma inu mwaiyesa phanga la acifwamba.
14 Ndipo anadza kwa Iye kuKacisiko akhungu ndi opunduka miyendo, naciritsidwa.
15 Koma ansembe akuru ndi alembi, m'mene anaona zozizwitsa zomwe Iye anazicita, ndi ana alinkupfuula kuKacisiko kuti, Hosana kwa Mwana wa Davide, anapsa mtima,
16 nanena kwa Iye, Mulinkumva kodi cimene alikunena awa? Ndipo Yesu ananena kwa iwo, Inde: simunawerenga kodi, M'kamwa mwa makanda ndi oyamwa munafotokozera zolemekeza?