21 Nanena iwo, Ca Kaisara. Pomwepo Iye anati kwa iwo, Cifukwa cace patsani kwa Kaisara zace za Kaisara, ndi kwa Mulungu zace za Mulungu.
22 Ndipo pamene iwo anamva, anazizwa, namsiya Iye, nacokapo.
23 Tsiku lomwelo anadza kwa Iye Asaduki, amene amanena kuti palibe kuuka kwa akufa; namfunsa Iye,
24 nanena, Mphunzitsi, Mose anati, Ngati munthu akafa wopanda mwana, mphwace adzakwatira mkazi wace, nadzamuukitsira mbale wace mbeu.
25 Tsono panali ndi ife abale asanu ndi awiri; ndipo wakuyamba anakwatira, namwalira wopanda mbeu, nasiyira mphwace mkazi wace;
26 cimodzimodzi waciwiri, ndi wacitatu, kufikira wacisanu ndi ciwiri.
27 Ndipo pomarizira anamwaliranso mkaziyo.