22 Ndipo wakulumbira kuchula Kumwamba, alumbira cimpando ca Mulungu, ndi Iye wakukhala pomwepo.
23 Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! cifukwa mupereka limodzi la magawo khumi la timbeu tonunkhira, ndi katsabola, ndi la citowe, nimusiya zolemera za cilamulo, ndizo kuweruza kolungama, ndi kucitira cifundo, ndi cikhulupiriro; koma zijazo munayenera kuzicita, osasiya izi zomwe.
24 Atsogoleri akhungu inu, akukuntha udzudzu, koma ngamila mummeza.
25 Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! cifukwa mutsuka kunja kwace kwa cikho ndi mbale, koma m'katimo iwo adzala ndi kulanda ndi kusadziletsa.
26 Mfarisi iwe wakhungu, yambotsuka m'kati mwa cikho ndi mbale, kuti kunja kwace kukhalenso koyera.
27 Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! cifukwa mufanafana ndi manda opaka njereza, amene aonekera okoma kunja kwace, koma adzala m'katimo ndi mafupa a anthu akufa ndi zonyansa zonse.
28 Comweco inunso muonekera olungama pamaso pa anthu, koma m'kati muli odzala ndi cinyengo ndi kusayeruzika.