1 Ndipo Yesu anaturuka kuKacisi; ndipo ophunzira ace anadza kudzamuonetsa cimangidwe ca Kacisiyo.
2 Koma Iye anayankha nati kwa iwo, Simuona izi zonse kodi? indetu ndinena kwa inu, Sipadzakhala pano mwala umodzi pa unzace, umene sudzagwetsedwa.
3 Ndipo pamene Iye analikukhala pansi pa phiri la Azitona, ophunzira anadza kwa Iye pa yekha, nanena, Mutiuze ife zija zidzaoneka liti? ndipo cizindikiro ca kufika kwanu nciani, ndi ca mathedwe a nthawi ya pansi pano?
4 Ndipo Yesu anayankha nati kwa iwo, Yang'anirani, asasokeretse inu munthu.
5 Pakuti ambiri adzafika m'dzina langa, nadzanena, Ine ndine Kristu, nadzasokeretsa anthu ambiri.
6 Koma inu mudzayamba kumva za nkhondo, ndi mbiri za nkhondo; onani, musadere nkhawa; pakuti kuyenera kuti izi zioneke; koma citsiriziro sicinafike.