27 cifukwa cace ukadapereka ndalama zanga kwa okongola ndalama, ndipo ine pobwera ndikadatenga zanga ndi phindu lace.
28 Cifukwa cace cotsani kwa iye ndalamayo, muipatse kwa amene ali nazo ndalama khumi.
29 Pakuti kwa yense amene ali nazo, kudzapatsidwa, ndipo iye adzakhala nazo zocuruka: koma kwa iye amene alibe, kudzacotsedwa, cingakhale cimene anali naco.
30 Ndipo ponyani kapoloyo wopanda pace ku mdima wakunja; kumene kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.
31 Koma pamene Mwana wa munthu adzadza mu ulemerero wace, ndi angelo onse pamodzi naye, pomwepo Iye adzakhala pa cimpando ca kuwala kwace:
32 ndipo adzasonkhanidwa pamaso pace anthu a mitundu yonse; ndipo Iye adzalekanitsa iwo wina ndi mnzace, monga mbusa alekanitsa nkhosa ndi mbuzi;
33 nadzakhalitsa nkhosa ku dzanja lace lamanja, koma mbuzi kulamanzere.