29 Pakuti kwa yense amene ali nazo, kudzapatsidwa, ndipo iye adzakhala nazo zocuruka: koma kwa iye amene alibe, kudzacotsedwa, cingakhale cimene anali naco.
30 Ndipo ponyani kapoloyo wopanda pace ku mdima wakunja; kumene kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.
31 Koma pamene Mwana wa munthu adzadza mu ulemerero wace, ndi angelo onse pamodzi naye, pomwepo Iye adzakhala pa cimpando ca kuwala kwace:
32 ndipo adzasonkhanidwa pamaso pace anthu a mitundu yonse; ndipo Iye adzalekanitsa iwo wina ndi mnzace, monga mbusa alekanitsa nkhosa ndi mbuzi;
33 nadzakhalitsa nkhosa ku dzanja lace lamanja, koma mbuzi kulamanzere.
34 Pomwepo Mfumuyo idzanena kwa iwo a ku dzanja lace lamanja, Idzani kuno inu odalitsika a Atate wanga, lowani mu Ufumu wokonzedwera kwa inu pa cikhazikiro cace ca dziko lapansi:
35 pakuti ndinali ndi njala, ndipo munandipatsa Ine kudya; ndinali ndi ludzu, ndipo munandimwetsa Ine; ndinali mlendo, ndipo munacereza Ine;