45 Pomwepo anadza kwa ophunzira, nanena kwa iwo, Gonani nthawi yatsalayi, mupumule; onani, nthawi yafika, ndipo Mwana wa munthu aperekedwa m'manja ocimwa.
46 Ukani, timuke; taonani, iye wakundipereka wayandikira.
47 Ndipo Iye ali cilankhulire, onani, Yudase, mmodzi wa khumi ndi awiriwo, anadza, ndi pamodzi ndi iye khamu lalikuru la anthu, ndi malupanga ndi mikunkhu, kucokera kwa ansembe akuru ndi akuru a anthu.
48 Koma wompereka Iye anawapatsa cizindikiro, nanena, Iye amene ndidzampsompsona ndiyeyo, mumgwire Iye.
49 Ndipo pomwepo anadza kwa Yesu, nati, Tikuoneni, Rabi; nampsompsonetsa.
50 Ndipo Yesu anati kwa iye, Mnzanga, wafikiranji: iwe? Pomwepo iwo anadza, namthira Yesu manja, namgwira Iye.
51 Ndipo onani, mmodzi wa iwo anali pamodzi ndi Yesu, anatansa dzanja lace, nasolola Iupanga lace, nakantha kapolo wa mkuru wa ansembe, nadula khutu lace.