48 Koma wompereka Iye anawapatsa cizindikiro, nanena, Iye amene ndidzampsompsona ndiyeyo, mumgwire Iye.
49 Ndipo pomwepo anadza kwa Yesu, nati, Tikuoneni, Rabi; nampsompsonetsa.
50 Ndipo Yesu anati kwa iye, Mnzanga, wafikiranji: iwe? Pomwepo iwo anadza, namthira Yesu manja, namgwira Iye.
51 Ndipo onani, mmodzi wa iwo anali pamodzi ndi Yesu, anatansa dzanja lace, nasolola Iupanga lace, nakantha kapolo wa mkuru wa ansembe, nadula khutu lace.
52 Pomwepo Yesu ananena kwa iye, Tabweza Iupanga lako m'cimakemo, pakuti onse akugwira lupanga adzaonongeka ndi Iupanga,
53 Kapena uganiza kuti sindingathe kupemphera Atate wanga, ndipo Iye adzanditumizira tsopano lino mabungwe a angelo oposa khumi ndi awiri?
54 Koma pakutero malembo adzakwaniridwa bwanji, pakuti kuyenera comweco?